Jump to content

Brussels

From Wikipedia
Brussels

Brussels (Braselozi) ndi dera lalikulu limene muli mizinda ingapo komanso tawuni yayikulu ya Brussels, imene ili likulu la dziko la Belgium. Brussels ndi dera limene muli anthu ambiri ku Belgium komanso ndi lolemela kuposa madera onse mudzikoli.

Brussels inakula kuchokera kudera laling'ono limene linali midzi yokha pa mtsinje wotchedwa Senne kufika kukhala tawuni yofunikila mu Ulaya. Kufikila nthawi yomwe nkhondo yadziko lonse yachiwiri inatha, mzindawu wakhala wofunika kwambiri pankhani za ndale ndipo ma bungwe ambiri anakhazikitsa likulu lawo kumeneko. Brussels ndi likulu la bungwe la European Union.

Brussels linali dera loyankhula chiDutch (chidatchi) koma linasintha kukhala dera loyankhula chiFrench (chifrenchi). Mudera limene muli likukulu mu tawuni ya Brussels, anthu amayankhula chidatchi ndi chifrenchi chomwe, ngakhale anthu ambiri padakali pano amayankhula chifrenchi. Chingerezi chimayankhulidwa ngati chiyankhulo chachiwiri komaso anthu ambiri obwera kudzagwira ntchito mderali amayankhula chingerezi.

Brussels imadziwika ndi zakudya zokoma zimene zimaphikidwa kudelali komanso nyumba zomangidwa bwino; ndipo nyumba zambiri ndizotetezedwa ndi a Unesco. Malo omwe ali okongola kukawona ndi grand place, Manneken Pis, Atomium ndi manyumba owonetsa mbiri ya dzikoli ndi ntchito zaluso.

Dziko : Belgium

Anthu opezeka ku Brussels: achiFrenchi ndi chiFlemish

chiwerengerero cha wanthu : 1,208,542

kukula kwa dera : 162.4 km2

Brussels