0% found this document useful (0 votes)
151 views7 pages

Chichewa Form 3

Uploaded by

preciouslivimbo1
Copyright
© © All Rights Reserved
We take content rights seriously. If you suspect this is your content, claim it here.
Available Formats
Download as DOCX, PDF, TXT or read online on Scribd

CHICHEWA FORM 3

(100 marks)

Gawo A (Malikisi 40)

Malamulo a Chiyankhulo

Langizo: Yankhani mafunso onse.

1. a. Pangani aonjezi ndi mawu otsatirawa.

(i) chinunu____________________________________

(ii) nong’ona___________________________________

(iii) tali________________________________________

(iv) nyengerera__________________________________
(v) dala. (Malikisi 10)

2. Fotokozani momwe mayina otsatirawa adapangidwidwira.

(i) kondaine

(ii) Langwani

(iii) Lamulo

(iv) njokaluzi

(v) gogoda

(10 marks)

3. Pangani afotokozi ndipo pangani ziganizo ndi afotokozi opangidwawo, kuchokera ku:
a. masinde enieni a mfotokozi
b. Kuchokera ku mayina

c. Kuchokera ku masinde ena

(15 marks)
4. Perekani zitsazo ziwiri za mitundu ya aneni otsatirawa:
a. Woyambukira

b. Wodalira

(5 marks)

Gawo B (Malikisi 20)

Kumvetsa Nkhani ndi Kusanthula Chiyankhulo

5. Werengani nkhani ili m’munsimu mosamala ndipo muyankhe mafunso otsatirawo.

Mayi Nagama adali womvetsa chisoni kwambiri zaka khumi zapitazo, amuna awo Bambo
Giligala atangotsamira mkono. Mayiyu adathedwa nzeru zitangochitika izi, poganizira mtolo
umene adayenera kuusenza yekhayekha. M’banja lawolo mudali Mphatso zisanu ndi imodzi
zomwe zidali zongopondanapondana mopanda kupatsidwa mpata [Link]
ankakhala ku tawuni ya Moyongokoma, Bambo Giligala ndi banja lawo adali kukhala moyo
wofewa. Adali kupeza zosowa zawo mosachita kugagada ndi nkhwangwa popeza bamboyu
adali kuchita malonda osiyanasiyana. Ndi chifukwa chake kugula nsalu yalekaleka chaka n’chaka
silidali vuto kwenikweni kwa iwo.

Ng’ombe zidayang’ana kungolo bamboyu atachita ngozi pamene adali kuchokera kopikula
malonda ake. Bamboyu adakhala ali pakama kwa miyezi yochuluka akubwira mtera
wosiyanasiyana kenako adatsinzina ali mchipatala cha Moyokunyenga. Pamene ankatsinzina
n’kuti chuma chonse [Link] kovuta kwambiri kuti Nagama ndi ana ake azolowere
moyo wakumudzi. Ndiye poti kadaona maso mtima suiwala, anawo anali kumuvutitsa mayiyo
kuti awapatse zomwe adali kudya kutawuni. Mitsinje idali kungodziyendera pa masaya a
ntchembereyi makamaka akasoweratu pogwira. Adayenera kuchitapo kanthu kuti mavutowo
achepe.
Chilimwe chitafika, adapempha kachigunda kotiazilimapo kachimanga kongokwanira banja
lakelo. Anzake anthanga yake adamulimbikitsa pomupatsa upangiri wothyakuka kuti sadali
yekhayo wosiyidwa m’mudzimo. Azimayi ambiri adali kuvina gule yemweyo. Motero Naga,
monga ambiri ankamuitanira, adagwira ntchito mwakhama ngati wothena agalu chaka
chimenecho.

Kwa nthawi yoyamba chimwalirire mwamuna wake adaona chiyembekezo ndi chimwemwe
zikumutsatira. Mbewu zidachita bwino ndipo adakolola chakudya chokwanira.

“Amayi, mangani malamba. Makamaka inu amayi amasiye, ikani mtima wanu pa chitukuko cha
maanja anu. Mungathe kukwaniritsa izi pochita ulimi. Udzasangula misozi yonse m’maso
mwanu.” Amayi onse adali chete kumvetsera pomwe mlangizi wazaulimi adali kulalika uthenga
wopatsa chiyembekezo.

“Mungathe kuchita ulimi wa mitundu itatu: wodalira mvula, wamthirira ndi waziweto. Ngati
muli ndi chidwi pa zomwe ndakambazi mutha kundiitanitsa mwapadera kuti ndikuunikireni
bwino za zonsezi.” Adatsiriza chotero bambo Makononjala ndipo pambuyo pake aliyense
adaona msana wa njira ya [Link] mutu kwa nthawi yaitali, Nagama adaganiza kuti
ayesere zomwe adamva zija podziwa kuti sikadza kokha kuopa kulaula. Adayamba ndi kulima
soya, mtedza ndi nyemba pothawa kugula feteleza. Adazisamalira bwino mbewu
[Link] adakolola matumba angapo ndipo zina adagulitsako. Ndalama zina
adagulirako feteleza ndi mbewu ya chimanga chamakono kuti ayesenso ulimi wamthirira.

Ulimi wamthirira udayendanso bwino. Adabzala chimanga chamakono, mnkhwani ndi nyemba.
Adazisamalira bwino chifukwa sadalole kuti mbewu zake zicheze ndi udzu mwa njira ina
iliyonse. Naga ndiye anali kupezetsa ndiwo anthu a kwa [Link] zake zidabereka
mwakholophethe zitadya nawo feteleza. Adazigulitsa pa mtengo wabwino kwambiri. Anthu
adali pikitipikiti kuzapikula dowe ku dimba la mayiyu, ena akutuluka ena akulowa. “Zoonadi
ndawapeza a Giligala, ali [Link] ndikwatirana ndi ulimi poti ana anga ayambanso
kusangalala,” adatero Nagama modziyankhulira ali kuwerenga ndalama zomwe adapeza
atapikulitsa chiamanga.

“Pafunika ndiyesenso [Link] nthawi kumangolira nthawi imene ija. Tsopano moyo
wanga wafewanso.”

Tsopano yankhani mafunso otsatirawa m’ziganizo zomveka bwino.

a.(i) Ndi ntchito iti yomwe Bambo Giligala ankagwira asanamwalire?
_________________________________________________________________________
________________________________________________________________(malikisi 1)
(ii) N’chifukwa chiyani ana ankavutitsa Nagama kuti awapatse chakudya chomwe adali kudya
kutawuni?
_________________________________________________________________________
________________________________________________________________(malikisi 1)
(iii) Tchulani mbewu ziwiri zakudimba zomwe zidampatsa Nagama makwacha ankhaninkhani.
_________________________________________________________________________
________________________________________________________________(malikisi 2)
(iv) Ndi chiyani chomwe Bambo Makononjala adanena kuti chidatha kutsangula misozi ya amayi
amasiye?
_________________________________________________________________________
________________________________________________________________(Malikisi 2)
(v) Kodi Nagama ankatanthauzanji ponena kuti “Zoonadi ndawapeza a Giligala, ali moyo”?
_________________________________________________________________________
______________________________________________________________________________
___________________________________________________________(Malikisi 2)

(vi) Ndi vuto lanji lomwe Nagama adali kusowa nalo mtendere mwamuna wake atamwalira?
_________________________________________________________________________
________________________________________________________________(Malikisi 2)

(vii)Fotokozani cholinga cha msonkhano womwe adachititsa a Bambo Makononjala.

_________________________________________________________________________
________________________________________________________________(Malikisi 2)

b. Kusanthula chiyankhulo
(i)Perekani matanthauzo a nsinjiro zachiyankhulo zotsatirazi molingana ndi momwe
zagwiritsiridwa ntchito munkhaniyi.
[Link] ________________________________________________________________(Malikisi
1)
[Link] kugagada ndi
nkhwangwa.________________________________________________________________(Mal
ikisi 1)
[Link]’ombe zidayang’ana
kungolo.________________________________________________________________(Malikisi
1)

[Link]
malamba________________________________________________________________(Malikis
i 1)
(ii)Pezani zining’a munkhaniyi zomwe matanthauzo ake ndi otsatirawa.
[Link]
________________________________________________________________(Malikisi 1)
[Link]
________________________________________________________________(Malikisi 1)
[Link]
________________________________________________________________(Malikisi 1)
[Link] wake
________________________________________________________________(Malikisi 1)
Gawo C (Malikisi 20)

Za Chikhalidwe
Langizo:Yankhani mafunso onse m’gawo ili.

6 (a) Werengani malonje ali m’munsiwa ndipo muyankhe mafunso otsatirawo:

“Achimwene , kugwira tambala pakamwa kumeneku, koma kumudzi kuli bwino? Komanso
mukuoneka kuti mwapha nyerere.”
“Ayi ndithu, sikuli bwino, kachere wagwa , Gogo Ndatsalapati atsamira dzanja usiku wathawu,
ndiye ndati ndidzakuchotseni malodza komanso poti mutu umodzi susenza denga,ndati
tidzagundane mitu pa dongosolo la zovutazi.” “Zikomo pondidziwitsa, koma angatifungatire
ndani tsopano achimwene popeza thambo lathu lagwa?”
(i) Malonjewa akuchitikira kuti?
___________________________________________________________________(Malikisi 1)
(ii) Ndi uthenga wanji womwe mlendoyu wabweretsa?
___________________________________________________________________
(Malikisi 1)
(iii) Malonjewa ndi a mtundu wanji? Nangakufunika kwake n’kotanii?
___________________________________________________________________
___________________________________________________________________
(Malikisi 2)
(iv)Pezani zinthuziwiri kuchokera mu malonjewa zomwe kufunika kwake kukufananitsidwa ndi
Gogo Ndatsalapati.
___________________________________________________________________
(Malikisi 2)
(v) Ndi mkuluwiko uti m’malonjemu womwe ukufanana m’matanthauzo ndi uwu:
“kalikokha n’kanyama, tilitiwiri n’tiwanthu”?
___________________________________________________________________
(Malikis 1)
(vi) Perekani matanthauzo a mawu otsatirawa:
1. Mwapha nyerere
___________________________________________________________________
___________________________________________________________________(Malikisi 2)
[Link] mitu
___________________________________________________________________
___________________________________________________________________(Malkisi 2)
[Link] wagwa
___________________________________________________________________
___________________________________________________________________(Malikisi 2)
[Link] tambala pakamwa
___________________________________________________________________
(Malikisi 2)
[Link] malangizo awiri ati okhudza uchembere wabwino omwe anthu angatsate?
___________________________________________________________________
___________________________________________________________________
___________________________________________________________________(Malikisi 2)
C. Tchulani zinthu zitatu zomwe zimapereka uthenga wozindikiritsa chikhalidwe cha anthu.
1. ________________________________________________________________
2. _________________________________________________________________
3. _________________________________________________________________ (Malikisi 3)
Gawo D (Malikisi 20)
Chimasuliro
7. Masulirani nkhani yotsatirayi m’Chichewa chomveka bwino.
EFFECTS OF CLIMATE CHANGE
Malawi is one of the most affected countries by climate change. This has negatively affected
agricultural production which is the economic backbone of the country. The impact of climate
change in Malawi is being manifested in various ways. These are intense rainfall, floods and
prolonged dry spells. People are living in poverty because they depend on good rains for food.
This poverty is now forcing some people to engage in immoral behaviour as a way of finding
money for food. This puts them at risk of contracting HIV and AIDS and other sexually
transmitted diseases.
________________________________________________________________________

MAFUNSO ATHERA PANO

You might also like